Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;
Masalimo 132:1 - Buku Lopatulika Yehova, kumbukirani Davide kuzunzika kwake konse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, kumbukirani Davide kuzunzika kwake konse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, mukumbukire Davide ndi mavuto onse amene adaŵapirira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, kumbukirani Davide ndi mavuto onse anapirira. |
Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa.
Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.