Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.
Masalimo 130:8 - Buku Lopatulika Ndipo adzaombola Israele ku mphulupulu zake zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo adzaombola Israele ku mphulupulu zake zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzaombola Israele ku machimo ake onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye mwini adzawombola Israeli ku machimo ake onse. |
Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.
Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.
Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.
Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.