Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano.
Masalimo 130:2 - Buku Lopatulika Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ambuye imvani liwu langa. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ambuye imvani mawu anga. Makutu anu akhale tcheru kumva kupempha chifundo kwanga. |
Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano.
Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.
Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.
Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo.
Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.
M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
Tcherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Senakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.