Masalimo 130:1 - Buku Lopatulika M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikulirira Inu Chauta, ndili m'dzenje lozama lamavuto. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama; |
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.
Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.
Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,