Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lake ilime m'mchera? Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa?
Masalimo 129:3 - Buku Lopatulika Olima analima pamsana panga; anatalikitsa mipere yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Olima analima pamsana panga; anatalikitsa mipere yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pondikwapula adani anga adachita ngati kulima pamsana panga, kulima mizere yaitali.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali: |
Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lake ilime m'mchera? Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa?
Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.
Ndidzachiika m'dzanja la iwo amene avutitsa iwe; amene anena kumoyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.