Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga.
Masalimo 128:3 - Buku Lopatulika Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako. |
Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga.
Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mivi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.
Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.
Kuti ana athu aamuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu aakazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.
Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.
Yehova anatcha dzina lako, Mtengo wa azitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikulu wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zake zathyoka.
Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, chifukwa cha madzi ambiri.
Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo wa azitona wa mtundu wakuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona?