Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
Masalimo 123:2 - Buku Lopatulika Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la mbuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Monga momwe anyamata amayang'anira ku dzanja la bwana wao, monga momwe adzakazi amayang'anira ku dzanja la dona wao, ndi momwenso timayang'anira ife kwa Chauta Mulungu wathu, mpaka atatichitira chifundo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo. |
Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye.
Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.
Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.
Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga.
Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.