Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;
Masalimo 122:9 - Buku Lopatulika Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu ndidzakufunira zokoma. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu ndidzakufunira zokoma. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa cha Nyumba ya Chauta, Mulungu wathu, ndidzakupemphera zabwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu, ndidzakufunira zabwino. |
Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;
Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.
Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.
Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse.
Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya; ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.
Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.