Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Masalimo 122:4 - Buku Lopatulika Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumeneko kumapita mafuko onse, anthu ake a Chauta, monga momwe adalamulira Israele kuti akayamike dzina la Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko, mafuko a Yehova, umboni wa kwa Israeli, kuti atamande dzina la Yehova. |
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe.
Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.
Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;
Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;