Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.
Masalimo 122:2 - Buku Lopatulika Mapazi athu alinkuima m'zipata zanu, Yerusalemu Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mapazi athu alinkuima m'zipata zanu, Yerusalemu Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mapazi athu akhala akuima m'kati mwa zipata zako, iwe Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mapazi athu akuyima mʼzipata zako, Iwe Yerusalemu. |
Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.