Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
Masalimo 121:7 - Buku Lopatulika Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako. |
Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.
Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.
Yehova aombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.
Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika padziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.
Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.