Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.
Masalimo 121:6 - Buku Lopatulika Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzuŵa silidzakupweteka masana, mwezi sudzakuvuta usiku. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana, kapena mwezi nthawi ya usiku. |
Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.
Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.
sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena chitungu chilichonse;