Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.
Masalimo 121:4 - Buku Lopatulika Taonani, wakusunga Israele sadzaodzera kapena kugona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taonani, wakusunga Israele sadzaodzera kapena kugona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi, amene amasunga Israele, ndithu sadzaodzera kapena kugona. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona. |
Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe.
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Pompo ndinapereka mtima wanga kudziwa nzeru, ndi kupenya ntchito zichitidwa pansi pano; kuti anthu saona tulo konse ndi maso ao ngakhale usana ngakhale usiku;
Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.
Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku mu Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,