Masalimo 121:1 - Buku Lopatulika Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti? |
Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.
Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele.