Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.
Masalimo 120:6 - Buku Lopatulika Moyo wanga unakhalitsa nthawi pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Moyo wanga unakhalitsa nthawi pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndakhala nthaŵi yaitali pakati pa anthu odana ndi mtendere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati pa iwo amene amadana ndi mtendere. |
Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.
Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.