Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu, pomchotsera moyo wake?
Masalimo 120:3 - Buku Lopatulika Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adzakuchitani chiyani, anthu onyenganu? Kodi adzakupatsani chilango cha mtundu wanji? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo? |
Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu, pomchotsera moyo wake?
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa.