kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.
Masalimo 12:7 - Buku Lopatulika Mudzawasunga, Yehova, mudzawatchinjirizira mbadwo uno kunthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzawasunga, Yehova, mudzawatchinjirizira mbadwo uno kunthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Titetezeni, Inu Chauta, titchinjirizeni nthaŵi zonse kwa anthu ameneŵa, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya. |
kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.
Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.
Kuopa Yehova kuli mbee, kwakukhalabe nthawi zonse; maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.
Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.
Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?
Inde akonda mitundu ya anthu; opatulidwa ake onse ali m'dzanja mwanu; ndipo akhala pansi ku mapazi anu; yense adzalandirako mau anu.
amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.
Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:
Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu.