Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.
Masalimo 12:6 - Buku Lopatulika Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Malonjezo a Chauta ndi angwiro, ali ngati siliva womkometsa m'ng'anjo yamoto, woyeretsedwa kasanunkaŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri. |
Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.
Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.
Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.
Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.
Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.
Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babiloni dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna, ati Yehova.