Masalimo 119:3 - Buku Lopatulika inde, sachita chosalungama; ayenda m'njira zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 inde, sachita chosalungama; ayenda m'njira zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa amene sachita zolakwa, koma amayenda m'njira za Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sachita cholakwa chilichonse; amayenda mʼnjira zake. |
koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.
naletsa dzanja lake pa wozunzika, wosalandira phindu kapena choonjezerapo, wochita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wake, adzakhala ndi moyo ndithu.
Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sangathe kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.
Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.