Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.
Masalimo 119:12 - Buku Lopatulika Inu ndinu wodala Yehova; ndiphunzitseni malemba anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu ndinu wodala Yehova; ndiphunzitseni malemba anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mutamandike Inu Yehova; phunzitseni malamulo anu. |
Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.
Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.
Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.
monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.
limene adzalionetsa m'nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye;
Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.