Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi khumbo lao lonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.
Masalimo 119:10 - Buku Lopatulika Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse; musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu. |
Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi khumbo lao lonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.
Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu.
Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse: Mundichitire chifundo monga mwa mau anu.
Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.
Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasochera m'menemo.
Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova.
Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika padziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.
Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;
Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye.
Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.