Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.
Masalimo 118:6 - Buku Lopatulika Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova ali nane; sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani? |
Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?
Tsiku lonse atenderuza mau anga, zolingirira zao zonse zili pa ine kundichitira choipa.
Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.
Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?
Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.
Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?
Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri.
Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.