Masalimo 118:25 - Buku Lopatulika Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano; tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano; tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tipulumutseni, tikukupemphani Inu Chauta. Chauta, tikukupemphani kuti zinthu zitiyendere bwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, tipulumutseni; Yehova, tipambanitseni. |
Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.
Ndipo chisomo chake cha Ambuye Mulungu wathu chikhalire pa ife; ndipo mutikhazikitsire ife ntchito ya manja athu; inde, ntchito ya manja athu muikhazikitse.