Masalimo 118:23 - Buku Lopatulika Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwitsa ichi pamaso pathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwitsa ichi pamaso pathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova ndiye wachita zimenezi ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu. |
Ichinso chifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wake uzizwitsa ndi nzeru yake impambana.
Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani; kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu, ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.
Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.