chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.
Masalimo 118:22 - Buku Lopatulika Mwala umene omangawo anaukana wakhala mutu wa pangodya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwala umene omangawo anaukana wakhala mutu wa pangodya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana wasanduka wapangodya; |
chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.
Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao.
Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?
Koma Iye anawapenyetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chinalembedwa, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unakhala mutu wa pangodya.
Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangodya.