Masalimo 118:21 - Buku Lopatulika Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha, ndipo munakhala chipulumutso changa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha, ndipo munakhala chipulumutso changa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikukuyamikani popeza kuti mwandiyankha, ndipo mwasanduka Mpulumutsi wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha; mwakhala chipulumutso changa. |
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la chipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;