Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Masalimo 118:19 - Buku Lopatulika Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsekulireni zipata za Nyumba ya Mulungu, kuti ndifike ku malo ake achilungamo, ndikathokoze Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsekulireni zipata zachilungamo, kuti ndifike kudzayamika Yehova. |
Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.
Yehova ndiye wondipulumutsa ine; Chifukwa chake tidzaimba nyimbo zanga, ndi zoimba zazingwe Masiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova.
Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.