Chifukwa chake tsono lupanga silidzachoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Muhiti akhale mkazi wako.
Masalimo 118:18 - Buku Lopatulika Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta wandilanga koopsa, koma sadandisiye kuti ndife. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova wandilanga koopsa, koma sanandipereke ku imfa. |
Chifukwa chake tsono lupanga silidzachoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Muhiti akhale mkazi wako.
Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.
Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.
monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;