Masalimo 118:17 - Buku Lopatulika Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova. |
Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.
Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu.
Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.
Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.
Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire mu Ziyoni ntchito ya Yehova Mulungu wathu.
Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.
Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.