Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Masalimo 118:14 - Buku Lopatulika Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa. |
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.