Masalimo 118:13 - Buku Lopatulika Kundikankha anandikankha ndikadagwa; koma Yehova anandithandiza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kundikankha anandikankha ndikadagwa; koma Yehova anandithandiza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adandikankha kwambiri, kotero kuti ndinali pafupi kugwa, koma Chauta adandithandiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anandikankha uku ndi uko ndipo ndinali pafupi kugwa, koma Yehova anandithandiza. |
Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
Mundichitire chizindikiro choti chabwino; kuti ondida achione, nachite manyazi, popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.
Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.
Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;
Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.
Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma Iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga chotuluka m'choponyera mwala.