Masalimo 116:3 - Buku Lopatulika Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Misampha ya imfa idandizinga, zoopsa za m'dziko la akufa zidandigwera. Ndidaona mavuto, nkugwidwa ndi nthumanzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zingwe za imfa zinandizinga, zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera; ndinapeza mavuto ndi chisoni. |
Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,