Masalimo 115:9 - Buku Lopatulika Israele, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Israele, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwe Israele, khulupirira Chauta. Chauta ndiye mthandizi wako ndi chishango chako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Aisraeli, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu. |
Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.
Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;
Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.