Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.
Masalimo 114:4 - Buku Lopatulika Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, timapiri ngati anaankhosa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, timapiri ngati anaankhosa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mapiri aakulu adalumphalumpha ngati nkhosa zamphongo, nazonso zitunda zidalumpha ngati anaankhosa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna, timapiri ngati ana ankhosa. |
Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.
Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?
Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.
Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.
Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.
Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.
Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.
Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje? Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi, kapena ukali wanu panyanja, kuti munayenda pa akavalo anu, pa magaleta anu a chipulumutso?
Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.