Masalimo 114:3 - Buku Lopatulika Nyanjayo inaona, nithawa; Yordani anabwerera m'mbuyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nyanjayo inaona, nithawa; Yordani anabwerera m'mbuyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nyanja idaona zimenezi nithaŵa, mtsinje wa Yordani udabwerera m'mbuyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nyanja inaona ndi kuthawa, mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo; |
Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inaphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu.
Madziwo anakuonani Mulungu; anakuonani madziwo; anachita mantha, zozama zomwe zinanjenjemera.
Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.
Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.
amene anayendetsa mkono wake waulemerero padzanja lamanja la Mose? Amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha?