Masalimo 113:8 - Buku Lopatulika Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu, pamodzi ndi akulu a anthu ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu, pamodzi ndi akulu a anthu ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amaŵakhazika pamodzi ndi mafumu, mafumu a anthu a Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amawakhazika pamodzi ndi mafumu, pamodzi ndi mafumu a anthu ake. |
Sawachotsera wolungama maso ake, koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.
M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi.
Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.
Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.