Masalimo 113:6 - Buku Lopatulika nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa wochita kuŵeramira pansi poyang'ana mlengalenga ndi dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amene amawerama pansi kuyangʼana miyamba ndi dziko lapansi? |
Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao.
Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.