Masalimo 113:1 - Buku Lopatulika Aleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake, tamandani dzina la Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Yehova. Mutamandeni, inu atumiki a Yehova, tamandani dzina la Yehova. |
Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku.
Yehova aombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.
Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira; ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m'mwemo.
Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang'ono ndi aakulu.