Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.
Masalimo 110:5 - Buku Lopatulika Ambuye padzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova pa dzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ambuye ali pambali pako. Adzaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ambuye ali kudzanja lako lamanja; Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake. |
Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.
Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo, munayera ngati matalala mu Zalimoni.
Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.
Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.
Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;
Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko.