Masalimo 109:7 - Buku Lopatulika Ponenedwa mlandu wake atuluke wotsutsika; ndi pemphero lake likhale ngati kuchimwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ponenedwa mlandu wake atuluke wotsutsika; ndi pemphero lake likhale ngati kuchimwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomuweruza apezeke kuti ali ndi mlandu, mapemphero ake akhale ngati kupalamula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene aweruzidwa, apezeke kuti ndi wolakwa, ndipo mapemphero ake amutsutse. |
Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.
Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;
Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.
Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;
Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi.