Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye.
Masalimo 109:6 - Buku Lopatulika Muike munthu woipa akhale mkulu wake; ndi mdani aime padzanja lamanja lake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muike munthu woipa akhale mkulu wake; ndi mdani aime pa dzanja lamanja lake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sankhulani munthu woipa kuti aweruze mlandu wa wondiwukirayo, iye aimbidwe mlandu ndi munthu woneneza anzake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sankhani munthu woyipa kuti amutsutse iye; lolani wotsutsa ayime ku dzanja lake lamanja. |
Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye.
nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.
Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende.
Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,
Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.