Inenso ndikadanena monga inu, moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga, ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu, ndi kukupukusirani mutu wanga.
Masalimo 109:25 - Buku Lopatulika Ndiwakhaliranso chotonza; pakundiona apukusa mutu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiwakhaliranso chotonza; pakundiona apukusa mutu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ondineneza amandinyodola, akandiwona amapukusa mitu yao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndine chinthu chotonzedwa kwa otsutsana nane; akandiona, amapukusa mitu yawo. |
Inenso ndikadanena monga inu, moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga, ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu, ndi kukupukusirani mutu wanga.
Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa, amlanditse tsopano popeza akondwera naye.
awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.
Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu,
Pakuti Khristunso sanadzikondweretse yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine.
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.