Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.
Masalimo 109:23 - Buku Lopatulika Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndazimirira ngati mthunzi wamadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe. |
Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.
Pamenepo Mose analoza ndodo yake padziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe.
Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.
Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?
koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.
inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.