Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 109:21 - Buku Lopatulika

Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Inu Mulungu, Ambuye anga, munditchinjirize malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, mundipulumutse chifukwa chikondi chanu chosasinthika ndi chabwino.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma Inu Ambuye Wamphamvuzonse, muchite nane molingana ndi dzina lanu, chifukwa cha ubwino wa chikondi chanu, pulumutseni.

Onani mutuwo



Masalimo 109:21
13 Mawu Ofanana  

Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.


Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.


Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.


Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.


Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.


Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa; chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje.


Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.


Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.


Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;