Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.
Masalimo 109:16 - Buku Lopatulika Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti munthuyo sadakumbukire kuchita chifundo, koma adazunza osauka, osoŵa ndi ovutika mu mtima, mpaka kuŵapha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo, koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka ndi osweka mtima. |
Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.
Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira.
Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.