Masalimo 109:15 - Buku Lopatulika Zikhale pamaso pa Yehova chikhalire, kuti adule chikumbukiro chao kuchichotsera kudziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zikhale pamaso pa Yehova chikhalire, kuti adule chikumbukiro chao kuchichotsera kudziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta asakhululukire machimowo mpaka muyaya, anthuwo aiŵalike pa dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Machimo awo akhale pamaso pa Yehova nthawi zonse, kuti Iye achotse chikumbutso chawo pa dziko lapansi. |
Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.
Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;
Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.
Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.
Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse ntchito zao zilizonse?