Masalimo 109:12 - Buku Lopatulika Pasakhale munthu wakumchitira chifundo; kapena kuchitira chokoma ana ake amasiye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pasakhale munthu wakumchitira chifundo; kapena kuchitira chokoma ana ake amasiye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima, kapena wina woŵachitira chifundo ana ake amasiye aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima kapena kumvera chisoni ana ake amasiye. |
Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; diso lao silidzaleka ana.
Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.
Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.