chilango chigwere pamutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya.
Masalimo 109:10 - Buku Lopatulika Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha; afunefune zosowa zao kuchokera m'mabwinja mwao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha; afunefune zosowa zao kuchokera m'mabwinja mwao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana ake azingoyendayenda nkumapemphapempha, apirikitsidwe m'mabwinja m'mene amakhala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha; apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo. |
chilango chigwere pamutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya.
Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.
Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.
Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.