Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Masalimo 108:8 - Buku Lopatulika Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga; ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga; ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga. Efuremu ali ngati chisoti changa chodzitetezera. Yuda ali ngati ndodo yanga yaufumu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu. |
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
Ku Hebroni anachita ufumu pa Yuda zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi; ndi ku Yerusalemu anachita ufumu pa Aisraele onse ndi Ayuda omwe zaka makumi atatu mphambu zitatu.
Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.
Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa.