Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.
Masalimo 108:5 - Buku Lopatulika Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu; ndi ulemerero wanu pamwamba padziko lonse lapansi, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu; ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu mumlengalenga monse. Wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba, ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi. |
Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.
Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi.
Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba padziko lonse lapansi.
Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.
Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.
Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.